Salimo 99
1 Yehova akulamulira,  
mitundu ya anthu injenjemere;  
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,  
dziko lapansi ligwedezeke.   
2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;  
Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.   
3 Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,  
Iye ndi woyera.   
   
 
4 Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo  
Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;  
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.   
5 Kwezani Yehova Mulungu wathu  
ndipo mulambireni pa mapazi ake;  
Iye ndi woyera.   
   
 
6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,  
Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;  
iwo anayitana Yehova  
ndipo Iyeyo anawayankha.   
7 Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;  
iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.   
   
 
8 Inu Yehova Mulungu wathu,  
munawayankha iwo;  
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,  
ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.   
9 Kwezani Yehova Mulungu wathu  
ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,  
pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.