Salimo 98
Salimo. 
 
1 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,  
pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;  
dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera  
zamuchitira chipulumutso.   
2 Yehova waonetsa chipulumutso chake  
ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.   
3 Iye wakumbukira chikondi chake  
ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;  
malekezero onse a dziko lapansi aona  
chipulumutso cha Mulungu wathu.   
   
 
4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,  
muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.   
5 Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,  
ndi zeze ndi mawu a kuyimba,   
6 ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna  
fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.   
   
 
7 Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,  
dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.   
8 Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,  
mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;   
9 izo ziyimbe pamaso pa Yehova,  
pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.  
Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,  
ndi mitundu ya anthu mosakondera.