Salimo 63
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. 
 
1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,  
moona mtima ine ndimakufunafunani;  
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,  
thupi langa likulakalaka inu,  
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa  
kumene kulibe madzi.   
   
 
2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika  
ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.   
3 Chifukwa chikondi chanu  
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.   
4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,  
ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.   
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.  
Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.   
   
 
6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu;  
ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.   
7 Chifukwa ndinu thandizo langa,  
ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.   
8 Moyo wanga umakangamira Inu;  
dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.   
   
 
9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;  
adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.   
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga  
ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.   
   
 
11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;  
onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,  
koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.