Salimo 64
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 
 
1 Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga;  
tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.   
2 Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa,  
ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.   
   
 
3 Iwo amanola malilime awo ngati malupanga,  
amaponya mawu awo olasa ngati mivi.   
4 Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa;  
amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.   
   
 
5 Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa,  
amayankhula zobisa misampha yawo;  
ndipo amati, “Adzayiona ndani?”   
6 Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati,  
“Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!”  
Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.   
   
 
7 Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi;  
mwadzidzidzi adzakanthidwa.   
8 Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa  
ndi kuwasandutsa bwinja;  
onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.   
   
 
9 Anthu onse adzachita mantha;  
adzalengeza ntchito za Mulungu  
ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.   
10 Lolani wolungama akondwere mwa Yehova  
ndi kubisala mwa Iye,  
owongoka mtima onse atamande Iye!