Salimo 62
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide. 
 
1 Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;  
chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.   
2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;  
Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.   
   
 
3 Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?  
Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,  
ngati mpanda wogwedezeka?   
4 Iwo akufunitsitsa kumugwetsa  
kuti achoke pa malo ake apamwamba.  
Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.  
Ndi pakamwa pawo amadalitsa  
koma mʼmitima yawo amatemberera.   
   
 
5 Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;  
chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.   
6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;  
Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.   
7 Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:  
Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.   
8 Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;  
khuthulani mitima yanu kwa Iye,  
pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.  
Sela
   
   
 
9 Anthu wamba ndi mpweya chabe;  
anthu apamwamba ndi bodza chabe;  
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;  
iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe   
10 Musadalire kulanda mwachinyengo  
kapena katundu wobedwa;  
ngakhale chuma chanu chichuluke,  
musayike mtima wanu pa icho.   
   
 
11 Mulungu wayankhula kamodzi,  
ine ndamvapo zinthu ziwiri;  
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,   
12 komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.  
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu  
molingana ndi ntchito zake.