Salimo 61
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe. 
 
1 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;  
mvetserani pemphero langa.   
   
 
2 Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu  
ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;  
tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.   
3 Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,  
nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.   
   
 
4 Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya  
ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.   
5 Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;  
mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.   
   
 
6 Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,  
zaka zake kwa mibado yochuluka.   
7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;  
ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.   
   
 
8 Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu  
ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.