Salimo 3
Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. 
 
1 Inu Yehova, achulukadi adani anga!  
Achulukadi amene andiwukira!   
2 Ambiri akunena za ine kuti,  
“Mulungu sadzamupulumutsa.”  
Sela
   
   
 
3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,  
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.   
4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula  
ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.  
Sela
   
   
 
5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo;  
ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.   
6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene  
abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.   
   
 
7 Dzukani, Inu Yehova!  
Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.  
Akantheni adani anga onse pa msagwada;  
gululani mano a anthu oyipa.   
   
 
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.  
Madalitso akhale pa anthu anu.  
Sela