Salimo 2
1 Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?  
Akonzekeranji zopanda pake anthu?   
2 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;  
ndipo olamulira asonkhana pamodzi  
kulimbana ndi Ambuye  
ndi wodzozedwa wakeyo.   
3 Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo  
ndipo titaye zingwe zawo.”   
   
 
4 Wokhala mmwamba akuseka;  
Ambuye akuwanyoza iwowo.   
5 Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake  
ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,   
6 “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga  
pa Ziyoni, phiri langa loyera.”   
7 Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:  
Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;  
lero Ine ndakhala Atate ako.   
8 Tandipempha,  
ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;  
malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.   
9 Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;  
udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”   
   
 
10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;  
chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.   
11 Tumikirani Yehova mwa mantha  
ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.   
12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;  
kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,  
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.  
Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.