Salimo 4
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. 
 
1 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,  
Inu Mulungu wa chilungamo changa.  
Pumulitseni ku zowawa zanga;  
chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.   
   
 
2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?  
Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?  
Sela.   
3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;  
Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.   
   
 
4 Kwiyani koma musachimwe;  
pamene muli pa mabedi anu,  
santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.  
Sela
   
5 Perekani nsembe zolungama  
ndipo dalirani Yehova.   
   
 
6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”  
Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.   
7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu  
kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.   
8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,  
pakuti Inu nokha, Inu Yehova,  
mumandisamalira bwino.