Salimo 23
Salimo la Davide. 
 
1 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.   
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,  
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,   
3 amatsitsimutsa moyo wanga.  
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo  
chifukwa cha dzina lake.   
4 Ngakhale ndiyende  
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,  
sindidzaopa choyipa,  
pakuti Inu muli ndi ine;  
chibonga chanu ndi ndodo yanu  
zimanditonthoza.   
   
 
5 Mumandikonzera chakudya  
adani anga akuona.  
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;  
chikho changa chimasefukira.   
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata  
masiku onse a moyo wanga,  
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova  
kwamuyaya.