Salimo 15
Salimo la Davide. 
 
1 Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?  
Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?   
   
 
2 Munthu wa makhalidwe abwino,  
amene amachita zolungama,  
woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,   
3 ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,  
amene sachitira choyipa mnansi wake  
kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,   
4 amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.  
Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,  
amene amakwaniritsa zomwe walonjeza  
ngakhale pamene zikumupweteka,   
5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja  
ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.  
   
 
Iye amene amachita zinthu zimenezi  
sadzagwedezeka konse.