Salimo 16
Mikitamu ya Davide. 
 
1 Ndisungeni Inu Mulungu,  
pakuti ine ndimathawira kwa Inu.   
   
 
2 Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga;  
popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”   
3 Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko,  
amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.   
4 Anthu amene amathamangira kwa milungu ina  
mavuto awo adzachulukadi.  
Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi  
kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.   
   
 
5 Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa;  
mwateteza kolimba gawo langa.   
6 Malire a malo anga akhala pabwino;  
ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.   
   
 
7 Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu;  
ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.   
8 Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.  
Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,  
sindidzagwedezeka.   
   
 
9 Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera;  
thupi langanso lidzakhala pabwino,   
10 chifukwa Inu simudzandisiya ku manda,  
simudzalola kuti woyera wanu avunde.   
11 Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;  
mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,  
ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.