Salimo 149
1 Tamandani Yehova.  
   
 
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,  
matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.   
   
 
2 Israeli asangalale mwa mlengi wake;  
anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.   
3 Atamande dzina lake povina  
ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.   
4 Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;  
Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.   
5 Oyera mtima asangalale mu ulemu wake  
ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.   
   
 
6 Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,  
ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,   
7 kubwezera chilango anthu a mitundu ina,  
ndi kulanga anthu a mitundu yonse,   
8 kumanga mafumu awo ndi zingwe,  
anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,   
9 kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo  
Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.  
   
 
Tamandani Yehova.