Salimo 148
1 Tamandani Yehova.  
   
 
Tamandani Yehova, inu a kumwamba,  
mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.   
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse,  
mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.   
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,  
mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.   
4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba  
ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.   
5 Zonse zitamande dzina la Yehova  
pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.   
6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;  
analamula ndipo sizidzatha.   
   
 
7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi,  
inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,   
8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,  
mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,   
9 inu mapiri ndi zitunda zonse,  
inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,   
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,  
inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.   
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,  
inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.   
12 Inu anyamata ndi anamwali,  
inu nkhalamba ndi ana omwe.   
   
 
13 Onsewo atamande dzina la Yehova  
pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;  
ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.   
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,  
matamando a anthu ake onse oyera mtima,  
Aisraeli, anthu a pamtima pake.  
   
 
Tamandani Yehova.