Salimo 147
1 Tamandani Yehova.  
   
 
Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu,  
nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!   
   
 
2 Yehova akumanga Yerusalemu;  
Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.   
3 Akutsogolera anthu osweka mtima  
ndi kumanga mabala awo.   
   
 
4 Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi,  
ndipo iliyonse amayitchula dzina.   
5 Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri;  
nzeru zake zilibe malire.   
6 Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa,  
koma amagwetsa pansi anthu oyipa.   
   
 
7 Imbirani Yehova ndi mayamiko;  
imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.   
8 Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo;  
amapereka mvula ku dziko lapansi  
ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.   
9 Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe  
ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.   
   
 
10 Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo,  
kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.   
11 Yehova amakondwera ndi amene amamuopa,  
amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.   
   
 
12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu;  
tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,   
13 pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako  
ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.   
14 Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako  
ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.   
   
 
15 Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi;  
mawu ake amayenda mwaliwiro.   
16 Amagwetsa chisanu ngati ubweya  
ndi kumwaza chipale ngati phulusa.   
17 Amagwetsa matalala ngati miyala.  
Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?   
18 Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka;  
amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.   
   
 
19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo,  
malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.   
20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;  
anthu enawo sadziwa malamulo ake.  
   
 
Tamandani Yehova.