Salimo 146
1 Tamandani Yehova.  
   
 
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.   
2 Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;  
ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.   
   
 
3 Musamadalire mafumu,  
anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.   
4 Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;  
zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.   
   
 
5 Wodala ndi amene thandizo lake ndi  
Mulungu wa Yakobo.   
6 Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,  
nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;  
Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.   
7 Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa  
ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.  
Yehova amamasula amʼndende,   
8 Yehova amatsekula maso anthu osaona,  
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,  
Yehova amakonda anthu olungama.   
9 Yehova amasamalira alendo  
ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,  
koma amasokoneza njira za anthu oyipa.   
   
 
10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,  
Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.  
   
 
Tamandani Yehova.