Salimo 130
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 
1 Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;   
2 Ambuye imvani mawu anga.  
Makutu anu akhale tcheru kumva  
kupempha chifundo kwanga.   
   
 
3 Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,  
Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?   
4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;  
nʼchifukwa chake mumaopedwa.   
   
 
5 Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,  
ndipo ndimakhulupirira mawu ake.   
6 Moyo wanga umayembekezera Ambuye,  
kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,  
inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,   
   
 
7 Yembekeza Yehova, iwe Israeli,  
pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika  
ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.   
8 Iye mwini adzawombola Israeli  
ku machimo ake onse.