Salimo 13
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 
 
1 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?  
Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?   
2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga  
ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?  
Mpaka liti adani anga adzandipambana?   
   
 
3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.  
Walitsani maso anga kuti ndingafe;   
4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”  
ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.   
   
 
5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;  
mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.   
6 Ine ndidzayimbira Yehova  
pakuti wandichitira zokoma.