Salimo 12
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide. 
 
1 Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;  
okhulupirika akusowa pakati pa anthu.   
2 Aliyense amanamiza mʼbale wake;  
ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.   
   
 
3 Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo  
ndi pakamwa paliponse podzikuza.   
4 Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;  
pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”   
   
 
5 “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu  
ndi kubuwula kwa anthu osowa,  
Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,  
“Ndidzawateteza kwa owazunza.”   
6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro  
monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,  
oyengedwa kasanu nʼkawiri.   
   
 
7 Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo  
mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.   
8 Oyipa amangoyendayenda ponseponse  
anthu akamayamikira zochita zawo.