Salimo 11
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 
 
1 Mwa Yehova ine ndimathawiramo.  
Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,  
“Thawira ku phiri lako ngati mbalame.   
2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;  
ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,  
pobisala pawo kuti alase  
olungama mtima.   
3 Tsono ngati maziko awonongeka,  
olungama angachite chiyani?”   
   
 
4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;  
Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.  
Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;  
maso ake amawayesa.   
5 Yehova amayesa olungama,  
koma moyo wake umadana ndi oyipa,  
amene amakonda zachiwawa.   
6 Iye adzakhuthulira pa oyipa  
makala amoto ndi sulufule woyaka;  
mphepo yotentha idzakhala yowayenera.   
   
 
7 Pakuti Yehova ndi wolungama,  
Iye amakonda chilungamo;  
ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.