Salimo 126
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 
1 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,  
tinali ngati amene akulota.   
2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;  
malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.  
Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,  
“Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”   
3 Yehova watichitira zinthu zazikulu,  
ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.   
   
 
4 Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,  
monga mitsinje ya ku Negevi.   
5 Iwo amene amafesa akulira,  
adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.   
6 Iye amene amayendayenda nalira,  
atanyamula mbewu yokafesa,  
adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,  
atanyamula mitolo yake.