Salimo 125
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 
1 Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,  
limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.   
2 Monga mapiri azungulira Yerusalemu,  
momwemonso Yehova azungulira anthu ake  
kuyambira tsopano mpaka muyaya.   
   
 
3 Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala  
pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,  
kuti anthu olungamawo  
angachite nawonso zoyipa.   
   
 
4 Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,  
amene ndi olungama mtima   
5 Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,  
Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.  
   
 
Mtendere ukhale pa Israeli.