Salimo 123
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 
1 Ndikweza maso anga kwa Inu,  
kwa Inu amene mumakhala kumwamba.   
2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo,  
monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake,  
choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu,  
mpaka atichitire chifundo.   
   
 
3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo,  
pakuti tapirira chitonzo chachikulu.   
4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza,  
chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.