Salimo 121
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 
1 Ndikweza maso anga ku mapiri;  
kodi thandizo langa limachokera kuti?   
2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova,  
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.   
   
 
3 Sadzalola kuti phazi lako literereke;  
Iye amene amakusunga sadzawodzera.   
4 Taonani, Iye amene amasunga Israeli  
sadzawodzera kapena kugona.   
   
 
5 Yehova ndiye amene amakusunga;  
Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.   
6 Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,  
kapena mwezi nthawi ya usiku.   
   
 
7 Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;  
adzasunga moyo wako.   
8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;  
kuyambira tsopano mpaka muyaya.