Salimo 113
1 Tamandani Yehova.  
   
 
Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,  
tamandani dzina la Yehova.   
2 Yehova atamandidwe,  
kuyambira tsopano mpaka muyaya.   
3 Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake,  
dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.   
   
 
4 Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse,  
ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.   
5 Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,  
Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?   
6 amene amawerama pansi kuyangʼana  
miyamba ndi dziko lapansi?   
   
 
7 Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi  
ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;   
8 amawakhazika pamodzi ndi mafumu,  
pamodzi ndi mafumu a anthu ake.   
9 Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake  
monga mayi wa ana wosangalala.  
   
 
Tamandani Yehova.