Salimo 114
1 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,  
nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,   
2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,  
Israeli anasanduka ufumu wake.   
   
 
3 Nyanja inaona ndi kuthawa,  
mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;   
4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,  
timapiri ngati ana ankhosa.   
   
 
5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?  
iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?   
6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,  
inu timapiri, ngati ana ankhosa?   
   
 
7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,  
pamaso pa Mulungu wa Yakobo,   
8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,  
thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.