13
Kuyeretsedwa ku Tchimo 
 
1 “Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.   
2 “Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa.  
3 Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.   
4 “Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.  
5 Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’  
6 Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’   
Kukantha Mʼbusa, Nkhosa Kubalalika 
 
7 “Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga,  
ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!”  
akutero Yehova Wamphamvuzonse.  
Kantha mʼbusa  
ndipo nkhosa zidzabalalika,  
ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.   
8 Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse,  
“zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka;  
koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.   
9 Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto;  
ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva  
ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide.  
Adzayitana pa dzina langa  
ndipo Ine ndidzawayankha;  
Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’  
ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”