12
Kuphedwa kwa Adani a Yerusalemu
Ulosi
1 Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti,
2 “Taonani, ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala chakumwa choledzeretsa chimene chidzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomuzungulira. Yuda adzazingidwa pamodzinso ndi Yerusalemu.
3 Pa tsiku limenelo, pamene mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi idzasonkhana kulimbana naye, ndidzasandutsa Yerusalemu thanthwe losatheka kusunthidwa ndi mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kumusuntha adzadzipweteka.
4 Pa tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamuchititsa mantha kuti asokonezeke, ndipo wokwerapo wake ndidzamuchititsa misala,” akutero Yehova. “Ndidzayangʼanira nyumba ya Yuda koma ndidzachititsa khungu akavalo onse a anthu a mitundu ina.
5 Pamenepo atsogoleri a Yuda adzayankhula mʼmitima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu ndi amphamvu, chifukwa Yehova Wamphamvuzonse ndiye Mulungu wawo.’
6 “Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake.
7 “Yehova adzapulumutsa malo okhala Yuda poyamba, kuti ulemu wa nyumba ya Davide ndi wa anthu okhala mu Yerusalemu usapambane ulemu wa Yuda.
8 Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera.
9 Pa tsiku limenelo ndidzawononga mitundu yonse yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu.
Kulirira amene Anamulasa
10 “Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa.
11 Pa tsiku limenelo mudzakhala kulira kwakukulu mu Yerusalemu, monga kulira kwa ku Hadadi-Rimoni ku chigwa cha Megido.
12 Dziko lidzalira kwambiri, fuko lililonse pa lokha, akazi awo pa okhanso: fuko la Davide pamodzi ndi akazi awo, fuko la Natani pamodzi ndi akazi awo,
13 nyumba ya Levi pamodzi ndi akazi awo, fuko la Simei pamodzi ndi akazi awo,
14 ndiponso mafuko onse pamodzi ndi akazi awo.