Salimo 95
1 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,  
tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu   
2 Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko  
ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.   
   
 
3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,  
mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.   
4 Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,  
ndipo msonga za mapiri ndi zake.   
5 Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,  
ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.   
   
 
6 Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,  
tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;   
7 pakuti Iye ndiye Mulungu wathu  
ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,  
ndi nkhosa za mʼdzanja lake.  
   
 
Lero ngati inu mumva mawu ake,   
8 musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,  
monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.   
9 Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,  
ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.   
10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;  
ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera  
ndipo sanadziwe njira zanga.”   
11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,  
“Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”