Salimo 69
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.” 
 
1 Pulumutseni Inu Mulungu,  
pakuti madzi afika mʼkhosi   
2 Ine ndikumira mʼthope lozama  
mʼmene mulibe popondapo.  
Ndalowa mʼmadzi ozama;  
mafunde andimiza.   
3 Ndafowoka ndikupempha chithandizo;  
kummero kwanga kwawuma gwaa,  
mʼmaso mwanga mwada  
kuyembekezera Mulungu wanga.   
4 Iwo amene amadana nane popanda chifukwa  
ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;  
ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,  
iwo amene akufunafuna kundiwononga.  
Ndikukakamizidwa kubwezera  
zomwe sindinabe.   
   
 
5 Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,  
kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.   
   
 
6 Iwo amene amadalira Inu  
asanyozedwe chifukwa cha ine,  
Inu Ambuye Wamphamvuzonse.  
Iwo amene amafunafuna Inu  
asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,  
Inu Mulungu wa Israeli.   
7 Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,  
ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.   
8 Ndine mlendo kwa abale anga,  
munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;   
9 pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa  
ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.   
10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya,  
ndiyenera kupirira kunyozedwa;   
11 pomwe ndavala chiguduli,  
anthu amandiseweretsa.   
12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,  
ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.   
   
 
13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,  
pa nthawi yanu yondikomera mtima;  
mwa chikondi chanu chachikulu  
Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.   
14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope,  
musalole kuti ndimire,  
pulumutseni ine kwa iwo  
amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.   
15 Musalole kuti chigumula chindimeze,  
kuya kusandimeze  
ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.   
16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;  
mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.   
17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,  
ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.   
18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;  
ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.   
   
 
19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,  
kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.   
20 Mnyozo waswa mtima wanga  
ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;  
ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,  
koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.   
21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa  
ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.   
   
 
22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;  
chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.   
23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso  
ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.   
24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo;  
mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.   
25 Malo awo akhale wopanda anthu  
pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.   
26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza  
ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.   
27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,  
musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.   
28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo  
ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.   
   
 
29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;  
lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.   
   
 
30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,  
ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.   
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,  
kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.   
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,  
Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!   
33 Yehova amamvera anthu osowa  
ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.   
   
 
34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,  
nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,   
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni  
ndi kumanganso mizinda ya Yuda,  
anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;   
36 ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,  
ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.