Salimo 58
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. 
 
1 Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama?  
Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?   
2 Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama,  
ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.   
3 Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera;  
kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.   
4 Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka,  
ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.   
5 Imene simva liwu la munthu wamatsenga,  
ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.   
   
 
6 Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu,  
Yehova khadzulani mano a mikango!   
7 Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda  
pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.   
8 Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda;  
ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.   
   
 
9 Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku,  
kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.   
10 Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango,  
pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.   
11 Ndipo anthu adzanena kuti,  
“Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho;  
zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”