Salimo 57
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga. 
 
1 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,  
pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.  
Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu  
mpaka chiwonongeko chitapita.   
   
 
2 Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,  
kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.   
3 Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,  
kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.  
Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.   
   
 
4 Ine ndili pakati pa mikango,  
ndagona pakati pa zirombo zolusa;  
anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,  
malilime awo ndi malupanga akuthwa.   
   
 
5 Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba;  
mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.   
   
 
6 Iwo anatchera mapazi anga ukonde  
ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa.  
Anakumba dzenje mʼnjira yanga  
koma agweramo okha mʼmenemo.   
   
 
7 Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu  
mtima wanga ndi wokhazikika.  
Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.   
8 Dzuka moyo wanga!  
Dzukani zeze ndi pangwe!  
Ndidzadzuka mʼbandakucha.   
   
 
9 Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu,  
ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.   
10 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba;  
kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.   
   
 
11 Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba,  
mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.