Salimo 54
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.” 
 
1 Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;  
onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.   
2 Imvani pemphero langa, Inu Mulungu  
mvetserani mawu a pakamwa panga.   
   
 
3 Alendo akundithira nkhondo;  
anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,  
anthu amene salabadira za Mulungu.   
   
 
4 Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;  
Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.   
   
 
5 Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;  
mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.   
   
 
6 Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;  
ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,  
pakuti ndi labwino.   
7 Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,  
ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.