Salimo 47
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. 
 
1 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;  
fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.   
2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;  
Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!   
3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;  
anayika anthu pansi pa mapazi athu.   
4 Iye anatisankhira cholowa chathu,  
chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.  
Sela
   
   
 
5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,  
Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.   
6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;  
imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.   
   
 
7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;  
imbirani Iye salimo la matamando.   
8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;  
Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.   
9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana  
monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,  
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;  
Iye wakwezedwa kwakukulu.