Salimo 46
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali. 
 
1 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,  
thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.   
2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,  
ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,   
3 ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,  
ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.   
   
 
4 Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,  
malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.   
5 Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;  
Mulungu adzawuthandiza mmawa.   
6 Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;  
Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.   
   
 
7 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,  
Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.   
   
 
8 Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,  
chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.   
9 Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;  
Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;  
amatentha zishango ndi moto.   
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;  
ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;  
ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”   
   
 
11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,  
Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.