Salimo 44
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.
Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu;
makolo athu atiwuza
zimene munachita mʼmasiku awo,
masiku akalekalewo.
Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena
ndi kudzala makolo athu;
Inu munakantha mitundu ya anthu,
koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
Sanalande dziko ndi lupanga lawo,
si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,
koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,
pakuti munawakonda.
 
Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga
amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu;
kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
Sindidalira uta wanga,
lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
koma Inu mumatigonjetsera adani athu,
mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse,
ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
 
Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa;
Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
10 Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani
ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
11 Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa
ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
12 Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika,
osapindulapo kanthu pa malondawo.
 
13 Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina,
chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
14 Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina;
anthu amapukusa mitu yawo akationa.
15 Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse
ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
16 chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe,
chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.
 
17 Zonsezi zinatichitikira
ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu
kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
18 Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo;
mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
19 Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe
ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.
 
20 Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu
kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21 kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi,
pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22 Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse,
tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
 
23 Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona!
Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24 Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,
ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
 
25 Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi;
matupi athu amatirira pa dothi.
26 Imirirani ndi kutithandiza,
tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.