Salimo 40
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 
 
1 Mofatsa ndinadikira Yehova  
Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.   
2 Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,  
mʼthope ndi mʼchithaphwi;  
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe  
ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.   
3 Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,  
nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.  
Ambiri adzaona,  
nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.   
   
 
4 Ndi wodala munthu  
amakhulupirira Yehova;  
amene sayembekezera kwa odzikuza,  
kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.   
5 Zambiri, Yehova Mulungu wanga,  
ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.  
Zinthu zimene munazikonzera ife  
palibe amene angathe kukuwerengerani.  
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,  
zidzakhala zambiri kuzifotokoza.   
   
 
6 Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,  
koma makutu anga mwawatsekula;  
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo  
Inu simunazipemphe.   
7 Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.  
Mʼbuku mwalembedwa za ine.   
8 Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;  
lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”   
   
 
9 Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;  
sinditseka milomo yanga  
monga mukudziwa Inu Yehova.   
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;  
ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.  
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu  
pa msonkhano waukulu.   
   
 
11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova;  
chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.   
12 Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira;  
machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona.  
Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga,  
ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.   
   
 
13 Pulumutseni Yehova;  
Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.   
14 Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga  
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;  
onse amene amakhumba chiwonongeko changa  
abwezedwe mwamanyazi.   
15 Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!”  
abwerere akuchita manyazi.   
16 Koma iwo amene amafunafuna Inu  
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;  
iwo amene amakonda chipulumutso chanu  
nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”   
   
 
17 Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa;  
Ambuye andiganizire.  
Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga;  
Inu Mulungu wanga, musachedwe.