Salimo 39
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide. 
 
1 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga  
ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;  
ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero  
nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”   
2 Koma pamene ndinali chete  
osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino  
mavuto anga anachulukirabe.   
3 Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,  
ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;  
kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:   
   
 
4 “Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga  
ndi chiwerengero cha masiku anga;  
mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.   
5 Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,  
kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;  
moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.  
Sela
   
6 Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:  
Iye amangovutika koma popanda phindu;  
amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.   
   
 
7 “Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?  
Chiyembekezo changa chili mwa Inu.   
8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;  
musandisandutse chonyozeka kwa opusa.   
9 Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga  
pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.   
10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;  
ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.   
11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;  
mumawononga chuma chawo monga njenjete;  
munthu aliyense ali ngati mpweya.  
Sela
   
   
 
12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova,  
mverani kulira kwanga kopempha thandizo;  
musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,  
popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;  
monga anachitira makolo anga onse.   
13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala  
ndisanafe ndi kuyiwalika.”