Salimo 19
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 
 
1 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;  
thambo limalalikira ntchito za manja ake.   
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,  
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.   
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;  
liwu lawo silimveka.   
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,  
mawuwo amafika mpaka  
kumalekezero a dziko lapansi.   
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,  
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.   
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo  
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;  
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.   
   
 
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro,  
kutsitsimutsa moyo.  
Maumboni a Yehova ndi odalirika,  
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.   
8 Malangizo a Yehova ndi olungama,  
amapereka chimwemwe mu mtima.  
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,  
amapereka kuwala.   
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,  
chimakhala mpaka muyaya.  
Maweruzo a Yehova ndi owona  
ndipo onse ndi olungama;   
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,  
kuposa golide weniweni;  
ndi otsekemera kuposa uchi,  
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.   
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;  
powasunga pali mphotho yayikulu.   
   
 
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?  
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.   
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;  
iwo asandilamulire.  
Kotero ndidzakhala wosalakwa,  
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.   
   
 
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga  
zikhale zokondweretsa pamaso panu,  
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.