Salimo 138
Salimo la Davide. 
 
1 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;  
ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”   
2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera  
ndipo ndidzayamika dzina lanu  
chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,  
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu  
kupambana zinthu zonse.   
3 Pamene ndinayitana, munandiyankha;  
munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.   
   
 
4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,  
pamene amva mawu a pakamwa panu.   
5 Iwo ayimbe za njira za Yehova,  
pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.   
   
 
6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,  
koma anthu onyada amawadziwira chapatali.   
7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,  
mumasunga moyo wanga;  
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,  
mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.   
8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;  
chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha  
musasiye ntchito ya manja anu.