Salimo 137
1 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira  
pamene tinakumbukira Ziyoni.   
2 Kumeneko, pa mitengo ya misondozi  
tinapachika apangwe athu,   
3 pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.  
Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;  
iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”   
   
 
4 Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova  
mʼdziko lachilendo?   
5 Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,  
dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.   
6 Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga  
ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,  
ngati sindiyesa iwe  
chimwemwe changa chachikulu.   
   
 
7 Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita  
pa tsiku limene Yerusalemu anagonja.  
Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi  
mpaka pa maziko ake!”   
   
 
8 Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,  
wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera  
pa zimene watichitira.   
9 Amene adzagwira makanda ako  
ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.