Salimo 134
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 
1 Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova,  
amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.   
2 Kwezani manja anu mʼmalo opatulika  
ndipo mutamande Yehova.   
   
 
3 Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,  
akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.