Salimo 110
Salimo la Davide. 
 
1 Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,  
“Khala ku dzanja langa lamanja  
mpaka nditasandutsa adani ako  
kukhala chopondapo mapazi ako.”   
   
 
2 Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;  
udzalamulira pakati pa adani ako.   
3 Ankhondo ako adzakhala odzipereka  
pa tsiku lako la nkhondo.  
Atavala chiyero chaulemerero,  
kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,  
udzalandira mame a unyamata wako.   
   
 
4 Yehova walumbira  
ndipo sadzasintha maganizo ake:  
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya  
monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”   
   
 
5 Ambuye ali kudzanja lako lamanja;  
Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.   
6 Adzaweruza anthu a mitundu ina,  
adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.   
7 Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;  
choncho adzaweramutsa mutu wake.