5
Chenjezo kwa Mkazi Wachigololo
Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi,
tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,
kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru
ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.
Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.
Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,
koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;
ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
Mapazi ake amatsikira ku imfa;
akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.
Iye saganizirapo za njira ya moyo;
njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.
 
Tsopano ana inu, mundimvere;
musawasiye mawu anga.
Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,
usayandikire khomo la nyumba yake,
kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;
ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,
10 kapenanso alendo angadyerere chuma chako
ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.
11 Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,
thupi lako lonse litatheratu.
12 Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!
Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13 Sindinamvere aphunzitsi anga
kapena alangizi anga.
14 Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke
pakati pa msonkhano wonse.”
 
15 Imwa madzi a mʼchitsime chakochako,
madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.
16 Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu?
Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?
17 Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha,
osati uyigawireko alendo.
18 Yehova adalitse kasupe wako,
ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
19 Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.
Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,
ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
20 Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?
Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
 
21 Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona,
ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.
22 Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha;
zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.
23 Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo,
adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.