Yoweli   
1
1 Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.   
Kubwera kwa Dzombe 
 
2 Inu akuluakulu, imvani izi;  
mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko.  
Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu,  
kapena mʼnthawi ya makolo anu?   
3 Muwafotokozere ana anu,  
ndipo ana anuwo afotokozere ana awo,  
ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.   
4 Chimene dzombe losamera mapiko lasiya  
dzombe lowuluka ladya;  
chimene dzombe lowuluka lasiya  
dzombe lalingʼono ladya;  
chimene dzombe lalingʼono lasiya  
chilimamine wadya.   
   
 
5 Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire!  
Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo;  
lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano,  
pakuti wachotsedwa pakamwa panu.   
6 Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa,  
wamphamvu ndi wosawerengeka;  
uli ndi mano a mkango,  
zibwano za mkango waukazi.   
7 Wawononga mphesa zanga  
ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu.  
Wakungunula makungwa ake  
ndi kuwataya,  
kusiya nthambi zake zili mbee.   
   
 
8 Lirani ngati namwali wovala chiguduli,  
chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.   
9 Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa  
sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova.  
Ansembe akulira,  
amene amatumikira pamaso pa Yehova.   
10 Minda yaguga,  
nthaka yauma;  
tirigu wawonongeka,  
vinyo watsopano watha,  
mitengo ya mafuta yauma.   
11 Khalani ndi nkhawa, inu alimi,  
lirani mofuwula inu alimi a mphesa;  
imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele,  
pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.   
12 Mpesa wauma  
ndipo mtengo wamkuyu wafota;  
makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,  
mitengo yonse ya mʼmunda yauma.  
Ndithudi chimwemwe cha anthu  
chatheratu.   
Mulungu Ayitana Anthu kuti Atembenuke 
 
13 Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani;  
lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe.  
Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse,  
inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga;  
pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa  
sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.   
14 Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya,  
itanani msonkhano wopatulika.  
Sonkhanitsani akuluakulu  
ndi anthu onse okhala mʼdziko  
ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu  
ndipo alirire Yehova.   
   
 
15 Kalanga ine tsikulo!  
Pakuti tsiku la Yehova layandikira;  
lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.   
   
 
16 Kodi chakudya chathu sichachotsedwa  
ife tikuona?  
Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu  
simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?   
17 Mbewu zikunyala  
poti pansi ndi powuma.  
Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka;  
nkhokwe zapasuka  
popeza tirigu wauma.   
18 Taonani mmene zikulirira ziweto;  
ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku  
chifukwa zilibe msipu;  
ngakhalenso nkhosa zikusauka.   
   
 
19 Kwa Inu Yehova ndilirira,  
pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo,  
malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.   
20 Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu;  
timitsinje tonse taphwa  
ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.