14
Kulapa Kubweretsa Madalitso 
 
1 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.  
Machimo anu ndi amene akugwetsani!   
2 Bweretsani zopempha zanu  
ndipo bwererani kwa Yehova.  
Munene kwa Iye kuti,  
“Tikhululukireni machimo athu onse  
ndi kutilandira mokoma mtima,  
kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.   
3 Asiriya sangatipulumutse;  
ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,  
sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’  
kwa zimene manja athu omwe anazipanga,  
pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”   
   
 
4 Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo  
ndipo ndidzawakonda mwaufulu  
pakuti ndaleka kuwakwiyira.   
5 Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli  
Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.  
Adzazika mizu yake pansi  
ngati mkungudza wa ku Lebanoni;   
6 mphukira zake zidzakula.  
Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,  
kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.   
7 Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.  
Iye adzakula bwino ngati tirigu.  
Adzachita maluwa ngati mphesa  
ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.   
8 Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?  
Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.  
Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;  
zipatso zako zimachokera kwa Ine.”   
   
 
9 Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.  
Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.  
Njira za Yehova ndi zolungama;  
anthu olungama amayenda mʼmenemo,  
koma anthu owukira amapunthwamo.