36
1 Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:   
2 “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani  
kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.   
3 Nzeru zanga ndimazitenga kutali;  
ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.   
4 Ndithudi mawu anga si abodza;  
wanzeru zangwiro ali ndi inu.   
   
 
5 “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu;  
Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.   
6 Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo  
koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.   
7 Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama;  
amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu  
ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.   
8 Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo,  
ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,   
9 Iye amawafotokozera zomwe anachita,  
kuti iwo anachimwa modzikuza.   
10 Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake  
ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.   
11 Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira,  
adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere,  
adzatsiriza zaka zawo mosangalala.   
12 Koma ngati samvera,  
adzaphedwa ndi lupanga  
ndipo adzafa osadziwa kanthu.   
   
 
13 “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo;  
akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.   
14 Amafa akanali achinyamata,  
pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.   
15 Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo;  
Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.   
   
 
16 “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso,  
kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani,  
kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.   
17 Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu;  
chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani.   
18 Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma;  
musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni.   
19 Kodi chuma chanu  
kapena mphamvu zanu zonse  
zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso?   
20 Musalakalake kuti usiku ubwere,  
pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka.   
21 Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo,  
chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu.   
   
 
22 “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu.  
Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?   
23 Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite,  
kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’   
24 Kumbukirani kutamanda ntchito zake  
zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.   
25 Anthu onse amaziona ntchitozo;  
anthuwo amaziona ali kutali.   
26 Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe!  
Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika.   
   
 
27 “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo,  
timene timasungunuka nʼkukhala mvula;   
28 mitambo imagwetsa mvulayo  
ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira.   
29 Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera,  
momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake?   
30 Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse,  
zimafika ngakhale pansi pa nyanja.   
31 Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu  
ndi kuwapatsa chakudya chochuluka.   
32 Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani,  
ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna.   
33 Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho;  
ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.