34
Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,
“Imvani mawu anga, inu anthu anzeru;
tcherani khutu inu anthu ophunzira.
Pakuti khutu limayesa mawu
monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.
Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera;
tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.
 
“Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa,
koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
Ngakhale ndine wolungama mtima,
akundiyesa wabodza;
ngakhale ndine wosachimwa,
mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’
Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani,
amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?
Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa;
amayanjana ndi anthu oyipa mtima.
Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu
poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’
 
10 “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu.
Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe,
Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.
11 Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake;
Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.
12 Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa,
kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.
13 Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani?
Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?
14 Mulungu akanakhala ndi maganizo
oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,
15 zamoyo zonse zikanawonongekeratu
ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.
 
16 “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi;
mvetserani zimene ndikunena.
17 Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira?
Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?
18 Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’
ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’
19 Iye sakondera akalonga
ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka,
pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?
20 Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku;
anthu amachita mantha ndipo amamwalira;
munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.
 
21 “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu;
amaona mayendedwe ake onse.
22 Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani
kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.
23 Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu,
kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
24 Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu
ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.
25 Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo
amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.
26 Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo,
pamalo pamene aliyense akuwaona;
27 Chifukwa anasiya kumutsata
ndipo sasamaliranso njira zake zonse.
28 Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake,
kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.
29 Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa?
Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe?
Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,
30 kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza,
kuti asatchere anthu misampha.
 
31 “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti,
‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,
32 ndiphunzitseni zimene sindikuziona
ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’
33 Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira,
pamene inu mukukana kulapa?
Chisankho nʼchanu, osati changa;
tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
 
34 “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana,
anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
35 ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru;
mawu ake ndi opanda fundo.’
36 Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto
chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
37 Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira;
amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu,
ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”