8
Israeli Akolola Kamvuluvulu 
 
1 “Ika lipenga pakamwa pako.  
Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova  
chifukwa anthu aphwanya pangano langa  
ndiponso agalukira lamulo langa.   
2 Israeli akulirira kwa Ine kuti,  
‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’   
3 Koma Israeli wakana zabwino;  
mdani adzamuthamangitsa.   
4 Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga.  
Amasankha akalonga popanda chilolezo changa.  
Amadzipangira mafano  
asiliva ndi agolide  
koma adzawonongeka nawo.   
5 Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!  
Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.  
Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?   
6 Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!  
Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;  
si Mulungu amene anamupanga.  
Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,  
mwana wangʼombe wa ku Samariya.   
   
 
7 “Aisraeli amadzala mphepo  
ndipo amakolola kamvuluvulu.  
Tirigu alibe ngala;  
sadzabala chakudya.  
Akanabala chakudya  
alendo akanadya chakudyacho.   
8 Israeli wamezedwa,  
tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina  
ngati chinthu cha chabechabe.   
9 Pakuti iwo anapita ku Asiriya  
ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha.  
Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.   
10 Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu,  
Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.  
Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa  
ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.   
   
 
11 “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo,  
maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.   
12 Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga,  
koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.   
13 Amapereka nsembe za nyama kwa Ine  
ndipo iwo amadya nyamayo,  
koma Yehova sakondwera nazo.  
Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo  
ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:  
iwowo adzabwerera ku Igupto.   
14 Israeli wayiwala Mlengi wake  
ndipo wamanga nyumba zaufumu;  
Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.  
Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,  
moto umene udzatenthe malinga awo.”