7
1 Pamene ndichiritsa Israeli,  
machimo a Efereimu amaonekera poyera  
ndiponso milandu ya Samariya sibisika.  
Iwo amachita zachinyengo,  
mbala zimathyola nyumba,  
achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.   
2 Koma sazindikira kuti Ine  
ndimakumbukira zoyipa zawo zonse.  
Azunguliridwa ndi zolakwa zawo;  
ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.   
   
 
3 “Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo,  
akalonga amasekerera mabodza awo.   
4 Onsewa ndi anthu azigololo,  
otentha ngati moto wa mu uvuni,  
umene wophika buledi sasonkhezera  
kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.   
5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu  
akalonga amaledzera ndi vinyo,  
ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.   
6 Mitima yawo ili ngati uvuni;  
amayandikira Mulungu mwachiwembu.  
Ukali wawo umanyeka usiku wonse,  
mmawa umayaka ngati malawi a moto.   
7 Onsewa ndi otentha ngati uvuni,  
amapha olamulira awo.  
Mafumu awo onse amagwa,  
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.   
   
 
8 “Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena;  
Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.   
9 Alendo atha mphamvu zake,  
koma iye sakuzindikira.  
Tsitsi lake layamba imvi  
koma iye sakudziwa.   
10 Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa,  
koma pa zonsezi  
iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake  
kapena kumufunafuna.   
   
 
11 “Efereimu ali ngati nkhunda  
yopusa yopanda nzeru.  
Amayitana Igupto  
namapita ku Asiriya.   
12 Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga;  
ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.  
Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi  
ndidzawakola.   
13 Tsoka kwa iwo,  
chifukwa andisiya Ine!  
Chiwonongeko kwa iwo,  
chifukwa andiwukira!  
Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa  
koma amayankhula za Ine monama.   
14 Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima,  
koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo.  
Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano,  
koma amandifulatira.   
15 Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa,  
koma amandikonzera chiwembu.   
16 Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba;  
ali ngati uta woonongeka.  
Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga  
chifukwa cha mawu awo achipongwe.  
Motero iwo adzasekedwa  
mʼdziko la Igupto.